Proverbs 26

1Ngati chisanu choti mbee nthawi yachilimwe kapena mvula nthawi yokolola,
ndi momwe zilili ndi ulemu wowulandira chitsiru.

2Ngati timba wokhalira kuwuluka kapena namzeze wokhalira kuzungulirazungulira,
ndi mmenenso limachitira temberero lopanda chifukwa, silichitika.

3Mkwapulo ndi wokwapulira kavalo, chitsulo ndi cha mʼkamwa mwa bulu,
choncho ndodo ndi yoyenera ku msana wa chitsiru.

4Usayankhe chitsiru monga mwa uchitsiru wake,
kuopa kuti ungadzakhale ngati chitsirucho.

5Koma nthawi zina umuyankhe monga mwa uchitsiru wake,
kuopa kuti angamadziyese yekha wanzeru.

6Kutuma chitsiru kuti akapereke uthenga
kuli ngati kudzidula mapazi ndipo kumakuyitanira mavuto.

7Monga miyendo ya munthu wolumala imene ilibe mphamvu
ndi mmene ulili mwambi mʼkamwa mwa chitsiru.

8Kupereka ulemu kwa chitsiru
zili ngati kukulunga mwala mʼlegeni.

9Monga umachitira mtengo waminga wobaya mʼdzanja la chidakwa
ndi mmene ulili mwambi mʼkamwa mwa chitsiru.

10Munthu amene amalemba ntchito chitsiru chongoyendayenda,
ali ngati woponya mivi amene angolasa anthu chilaselase.

11Chitsiru chimene chimabwerezabwereza uchitsiru wake
chili ngati galu amene amabwerera ku masanzi ake.

12Munthu wa uchitsiru aliko bwino popeza pali chiyembekezo
kuposana ndi munthu amene amadziyesa yekha kuti ndi wanzeru.

13Munthu waulesi amati, “Mu msewu muli mkango,
mkango woopsa ukuyendayenda mʼmisewu!”

14Monga chitseko chimapita uku ndi uku pa zolumikizira zake,
momwemonso munthu waulesi amangotembenukatembenuka pa bedi lake.

15Munthu waulesi akapisa dzanja lake mu mʼbale;
zimamutopetsa kuti alifikitse pakamwa pake.

16Munthu waulesi amadziyesa yekha wanzeru
kuposa anthu asanu ndi awiri amene amayankha mochenjera.

17Munthu wongolowera mikangano imene si yake
ali ngati munthu wogwira makutu a galu wongodziyendera.

18Monga munthu wamisala amene
akuponya sakali zamoto kapena mivi yoopsa,
19ndi momwe alili munthu wonamiza mnzake,
amene amati, “Ndimangoseka chabe!”

20Pakasowa nkhuni, moto umazima;
chomwechonso pakasowa anthu amiseche mkangano umatha.

21Monga alili makala pa moto wonyeka kapena mmene zimachitira nkhuni pa moto,
ndi mmene alili munthu wolongolola poyambitsa mikangano.

22Mawu a munthu wamiseche ali ngati chakudya chokoma;
chimene chimatsikira mʼmimba mwa munthu.

23Monga mmene chiziro chimakutira chiwiya chadothi
ndi mmene mawu oshashalika amabisira mtima woyipa.

24Munthu wachidani amayankhula zabwino
pamene mu mtima mwake muli chinyengo.
25Ngakhale wotereyu mawu ake ali okoma, koma usamukhulupirire,
pakuti mu mtima mwake mwadzaza zonyansa.
26Ngakhale amabisa chidani mochenjera,
koma kuyipa kwakeko kudzaonekera poyera pa gulu la anthu.

27Ngati munthu akumba dzenje, adzagweramo yekha;
ngati munthu agubuduza mwala, udzamupsinja iye mwini.

28Munthu wonama amadana ndi amene anawapweteka,
ndipo pakamwa poshashalika pamabweretsa chiwonongeko.
Copyright information for NyaCCL